April 18, 2020 - Hits: 47.2K file_download : 29.4K

format_align_center Song Lyrics


Verse 1(HB)
 Ndikangodzuka mamawa
chomwe ndimadziwa n'kupeza dollar//
Ola🕰️ yanga imathera pazibawa🍺kapena daily kumangosuta zichamba🚬//
Akazi kumangosintha// ndipo kupemphera n'mati sin'tha//
Zanga akandiuza HB sintha Moyo wako ndimati sinthawi //
Osandiuzano chochita osandiuzano kopita nthawi ndi yanga //
Osandipatsano manjenje ingosungirani mpweyawo puma mphwanga //
osachita zanga mphwanga olo Apo ndikutema ndipanga🔪 //
osandiuza za Gahena ngati Paul Apo nde ndikutema//
ndilibe nyali  ndeno ndilibe nthawi yoziunikira ndekha
ndimafuna nditasintha  koma ndikanena  anzanga amandiseka//
kundinyoza kokhakokha//
ndimpake nthawi zambiri ndimangogiva// kundikhola mumandikhola koma ineyo sindizimva//
mzimu wanga ukufuna koma thupi lokha fever//
Ndeno mwangobwera nokha//
mtima wanga ndikukonza
chilichonse ndikukonza
Uzimu wanga ndikukonza//
Mwandisankha ndinu Yahweh nde panopa singathawe//
Ndikuchita zamachawi
mopikisana ndi nthawi//
Palibe mbwerera
ndabwerera
pamaso panu ndi yeretseni.....

aaaaaaah 😝😝😝
  Hook(Leslie & HB)

Funa ndilape
Kubwerera kwa Inu mbuye
Munditsukene
(Mundiyeretse eeeeh ×)
Ndipo Moyo wanga wayeraaaaaa
Mbeee mbeee mbeee
Ndayeretsedwa ukandiona ndikuwalane  ndayeretsedwa
Mbee mbee mbee
Ndimwazi wa Yehova wo Ndayeretsedwa
Mbeee mbeee mbeee

Mbee mbee mbee

Ndayeretsedwaaaa

Verse. 2 HB

 Ndeno nditazifufuza ndinaona kuti zonsezi mzachabe//
Ndimaziduduluza muuchimo Moyo wanga unali shabby//
Ndimayenera kumufufuza Yesu Khristu kuti andichape//
Zimachimozi ndilape ,Mudzina lake nso ndi Rappeee//
Palibenso kutopa whuuuu  haaa

Mphamvu ya Yehova yomwe timatama //
Okamba amatinena kuti ndife amatama//
Koma timalimbikira Ife tili ndizikhama//
Sitibwereranso mmbuyo Ife tikuchilimika ,tikukhazikika,sitibaizika//
Muchi Khristu chathu tikuyaka Moto🔥 osapola chamba osabhola //
Uchimo ukabwera tingotchola// paliponse osalola ungolowaa//

Ndine waukali heavy😡😡aaaah
Msilikali waku Heaven ,ndimapreacher sindigona nane m buku lanu mundilembe//
Popeza mwanditsimikizira ndikatsata Inu Moyo wanga uli tayale //
Simudzalola kuti  devil 😈 abwere mavuto pa moyo wanga ayale //
Ndikakhala pansi neh (ahaa)
Kuganizira neh (aha)
Moyo wanga kale neh(aha)
Ndinkangolira neh(aha)
Nzanga chimene wakukonzera Yahweh dziwa sichingathawe//
Aliyense Ali ndi ndinthawi
Dzuka nawe  chita machawi ,tiye yenda usatsale m'bale weee aaaaaah😝😝

 


playlist_play HB Singles

Featured Music

© 2020, Malawi Media Network
Aurtial inc