Feb. 12, 2021 - Hits: 2.7K file_download : 1.9K

format_align_center Song Lyrics


Mmmh....Mmmmhh

V.1 (A'chanza)
Muse....
Aah iwe Nachanza
mkazi odzala ndi Chikondi iwe opanda Nkhanza
Kukhala nawe cha pafupi nimazifira Panza
Ine gwede-gwede ndimatama pamaso panza..nga
Umatha bwanji ogooo!
ka verbal fight umakamalizira pa mawondo
U pray for us osagonja umandigwira mkono
Kundilera ngati baby ine pheee ndi mkonono
Kumphika kwa khalidwe mkazi ndiwe mpoto
Landira ulemu ngati student polowa ku Portal
U straighten me nkapendama ndili poto-poto
Ambuye ndithu atalenga iweyo anadzipatsa mphoto
Kuthamangitsa udzudzu ndiwedi mpungabwi
Ntimano tako tili mbee ngati Mpunga bwi-
-no kumasamala Mammie ansanjewa ndi ochuluka
Ambuye patsogolo polowa ndi potuluka
Nachanza ndiwe ngenge no makani nde
Udandimata ndi chikondi dothi la Makande
Za khalidwe lako palibe angamake
Ndiwe chiphadzuwa chenicheni makamaka eti


CHORUS
Ndakusowa Mkazi wanga
Iwe mkazi wanga


V.2 (Salimo)
Ukakhala kutali
Ndimakhala Ngati mlendo
Ndimasowa chikondi Chako
Ndi kufunda Kwa thupi lako

Ukakhala kutali nane
ndimakhala Ngati mlendo
Ndimasowa chikondi chako
ndi kufunda Kwa thupi lako

Ndimalota tili pakhonde
Gitala ili mmanja
Ndikuimba tinyimbo tokoma
Kusangulusa duwa langa

Ndimalota tili pakhonde
Nsambo zili mmanja
Watching the kids play together
While I play you a song

CHORUS
Ndakusowa mkazi wanga
Iwe mkazi wanga


BRIDGE
(Salimo)
These are the memories i keep (Ndibwera Ndibwera)
These are the melodies i sing (Ndibwera ndibwera)
Ndikuimba tinyimbo tokoma
Kusangulutsa duwa langa

(A'chanza)
Will u be mine 4eva ili funso
Ndiuze pano usagonereze mfutso
Ndufuna yankho lako lero ndi full stop
Usalowe khomo lachibwana Fools door


playlist_play A'Chanza Singles

Featured Music

© 2020, Malawi Media Network
Aurtial inc